Rev. Ron Hanko
Mphatso za atumwi Mwa zina mwa izo ndi izi kulankhula ma Malirime, Kuchita zozizwa komanso kuchilitsa (Onse omwe amalimbikitsa mphatso zotchedwa kuti, “Madalitso aku Tolonto” amanena kuti ali ndi ulamuliro wa Atumwi Pa
mchitidwe wachisonezo monga uwu Phwete la ku Uzimu ndi kuphwedwa mu uzimu.) Kodi tikuyenera kuyembekeza
ndikupemphera kuti Mphatso zimezi zikhoza kuwonera mu nthawi yathu ino?
Timakhulupilira kuti Mphatso monga zimenezi, Mphatso za Mzimu wa Mulungu, Zidasiya kugwira ntchito kuchokera Nthawi imene ophuzira A yesu adamwalira komanso ndi nthawi imene malemba a M’bukhu loyera anamalizidwa kulembedwa ndikupatulidwa. Ngati Mphatso zimenezi zikupitira ngati siziri zongoganizira kapena zachinyengo chabe, ndekuti ndi ntchito ya Mizimu ina osati Mzimu Oyera (11 Ates 2:9).
Tikuyankhula zimenezi mogwilizana ndi Malemba.
Malemba amazitcha Mphatso zonsezi kuti, “Zizindikiro za Atumwi’’ ku 2 Akolinto 12:12. Zimenezi zikutanthawuza kuti Mphatso zimenezi ndi za Mthawi ya Atumwi. Muchowona cheni cheni, palibe pomwe panalembadwa mu M’mawu amulungu Mphatsozi zikupelekwedwa kwa wina aliyense Osakhala Atumwi, Makamaka ku Buku la (Machitidwe Atumwi. 8:14-17) Umboni uwu ukukuyenera kukhala okwanira kuti zinasiya kugwira ntchito kuyambira nthawi yomwe Atumwi ose adamwalira.
Mwanjira ina, kukhulupilira ndi kufunafuna kuti Mphatsozi zipitilire ndikusavomeleza kuti Mawu Amulungu ndi Okwanira (Tim. 3:16-17, Chivumbulutso 22:18-19).
Chivomelezo cha Chikhulupiliro Cha Westmister Chimati “Mawu onse Amulungu okhudzana ndi zinthu zonse zofunika
pa ulemelero wake, Chipulumutso cha Munthu, Chikhulupiliro ndi Moyo, zinalembedwa Mmalemba. Kapena kuti zabwino, ndi zotsatira za zinthu zonse zofunikira zimayenera kuchokera M’malemba . Kotero kuti pa nthawi
inailiyonse sipakufunikira kuwonjera zomwe zinalembedwa kale, kaya kudzera Chivumbulutso cha Mzimu kungakhalenso zikhulupiliro za wanthu” (1.7).
Mphatso izi Zinapatsidwa ngati zizindikiro komanso umboni omwe udzawatsate pa nthawi yomwe Atumwi
akumphunzitsa ndi kulalikira, pa Mthawi imene Malemba opatulika asanamalizidwe kulembedwa ndikupatulidwa (Heb. 2:3-4) . Tsopano chifukwa chakuti tili ndi Buku lopatulika la Mawu Amulungu lomwe linamalizidwa kulembedwa, lowuzilidwa ndi M’pweya wake komanso losalakwitsa, Sitikufunikanso zizindikiro zimenezi. Ngati tipemphanso kuti Mphatso zimenezi zibwelelere ziwonetsa kuti tikukana mawu amulungu kuti ndi Okwanira nthawi zonse.
Onsati zokhazo, Koma mawu amulungu amatiwuza kuti ndiopambana kuponsa zinthu zonsezi. Mongosiyanitsanso
Makamaka Pakumowona Yesu , kungakhalenso nthawi imene adasandulika pa Phiri. Malemba Amulungu ndi Mawu
“otsimikizikadi koposa” (2 Petulo 1:19). Tiyeni timvere malemba osati tifunefune Kubwelera kwa Mphatso za Atumwi. Mawu amulungu ndiothekera “kutipanga kukhala anzeru pa chipulumutso chakudza kudzera mu Chikhulupiro Cha mwa yesu Nkhrisitu.” Tisowanso chani?