Rev. Ron Hanko
Timakhulupira Chilango Chamuyaya, kuti onse omwe salapa Tchimo ndi kukhulupilira mwa Yesu Khristu pa chipulumutso Adzazunzika pa Chilango cha muyaya ku malo otchedwa kuti Gehena.
Kodi Mchifukwa chani timakhulupilira pa Chinthu chowopswa ngati ichi?
(1) Baibulo limaphunzitsa zokhudzana ndizimenezi. Mateyu 25:46 imati, “Amenewa adzapita kuchilango chosatha pamene olungama ku Moyo wosatha.” Chivumbulutso 14:11 imati “ndipo utsi wamoto wowazunzawo udzakwera kumwamba mpaka muyaya: sikudzakhala kupumula usana ndi usiku kwa aliyense amene anapembedza Chilombo chija ndi fano lake kapena kwa aliyense amene analembedwa chizindikiro cha dzina lake lija.”
(2) Chilungamo cha Mulungu ndichofunitsitsa kuti chilangochi chikachitike. Anthu onse ndiosamvera Mulungu monga zikuwonekera, kuti anthu ambiri sasamara zamulungu ndi Mawu ake, sichi chilango chabe cha Muyaya koma Mulungu otilenga ife adzakhala akubwezera onse omuchimwira iye.
(3) Mtanda uja ndi imfa ya Yesu Mkhrist ndizopanda Phindu ngati anthu savomereza kuti kuli Chilango cha Muyaya, chifukwa chakuti palibe chomwe chikupangitsa kuti munthu ochimwa apulumutsidwe kapena kuti sipafunikiranso kuti anthu apulumutsidwe Chifukwa sakulowera kunjira yopita ku Gahena. Ngati Gehena kulibe Lamulo limene likupezeka muwuthenga wabwino kuti anthu Alape komanso kuti anthu adzawonongeka ndiye kuti Lamulori ndi labodza, Chifukwa cha ichi anthu sakuyenera kulapa kapena kukhulupilira uthenga wabwino wa yesu khrist. Mwina nkutheka muli M’gulu la anthu omwe simukhulupilara kuti kuli Gehena kapena simukhulupilira mwa Yesu khristu.
Buku lopaturika limayankhura zokhudzana ndi Gehena osati mokuopsezani kuti munjenjemere ndi mantha opanda chidziwitso, koma kuti munjenjemere ndi mantha okhara ndi chidziwitso (Akorinto 4:11) ndikukuwonetsa kufunika koti mukhulupilire mwa Iye.
Kulibe amene amawopa Chilango kapena kutha kwa Moyo kumene sikukhudzana ndi mazuzo amuyaya.
Munthu wina odziwikabwino amene sakhulupilira kuti kuli Mulungu anati “pali Chinthu chimodzi Chimene chimandipangitsa kukhara jenkha pa zonse zokondweletsa Moyo wanga … ndimachita mantha chifukwa Baibulo ndilowona ,ngati ndimadziwiratu kuti Imfa ndi tulo ta muyaya, Ndikuyenera kukhara okondwera – chimwemwe changa chikuyenera kukhara chokwanira. Koma … ngati Baibulo ndilowona, ndine Otayika mpaka kale. Chiyembekezo changa chonse ndichotayika ndipo ndine otayika mpaka Muyaya.”
Kodi kwa Muyaya amathandawuzadi kuti “Mpaka Kalekale?”
Inde amathandawuza choncho, Ku Mateyu 25:46 Mawu amenewa anagwilitsidwa ntchito pakufutokozera Chilango cha Muyaya cha anthu ochimwa ku Gehena, komanso Mdalitso wa anthu olungama kumwamba. Ngati Gehena ndi Chilango chake sichamuyaya ndiye kutinso kumwamba ndi Mdalitso wake sizamuyaya. Wina aliyense amene amakhulupilira Moyo wamuyaya wakumwamba sakuyenera kunena kuti Gehena kulibe.
Anthu ambiri amakhulupilira motelemu, makamakanso kwa iwo omwe amanena kuti amakhulupilira Baibulo, zizindikiro zomwe zimkawonekera kwa anthu omwe si akhristu zayamba kuwonekera kwa anthu omwe akutchedwa kuti ndi akhristu lero, mwachitsanzo Baibulo latsopano lomwe lidatanthawulizidwa ndi a “New International Version” lamuchingelezi, Baibulo lomwe limagwiritsidwa ntchito ndi Akhristu ambiri otchedwa kuti Evangelicals, adachotseratu mawu akuti Gahena kuyambira muchipangano cha Kale komanso pafupifupi chipangano Chatsopano. Izi zikuyenera kutsutsidwa, ndiponso zizikusintha umboni weniweni omwe uli mu Buku Lopatulika.
Tikuyenera kufunsa kuti timve maganizo anu zokhudzana ndi chiphunzitso chimwenechi. Kodi mukhulupilira chomwe mulungu akuyankhura mu Mawu ake zokhudzana ndi Malo owopsawa otchedwa kuti Gahena? Ngati simukhulupira chonde khalani ndi nthawi yolingalira za zimenezi chifufwa mukuziika pachiwopsezo chopita ku Malo owopsa ngati amenewa. Kukana Gehena kapena Chilango chosatha, ndikukana chiphunzitso chowona chomwe chili mu Baibulo. Kukana chimphunzitso chowonadi chomwe chiri mu Baibulo ndikukhara munthu wabodza (1 Yohane 2:22) ndipo wina aliyense wabodza sakalowa mu Ufumu waku Mwamba (Chibvumbulutso 21:27).