Menu Close

Chifundo ndi chiweruzo pa Israeli / Mercy and Judgment Upon Israel

     

Rev. Ron Hanko

Mawu opezeka ku Numeri 14 amagwilitsidwa ntchito ndi anthu ena pomphuzintsa Chifundo cha Mulungu chapa anthu omwe sadzapulumutsidwa, “Yehova sakwiya nsanga ndipo ndiwodzadza ndichikondi chosasinthika, wokhululukira ntchimo ndikuwukira. Koma iye sadzaleka kulanga ochimwa, iye amalanga ana chifukwa cha Tchimo lamakolo awo kufikira m’badwo wachitatu ndi chinayi, chifukwa kwakukura kwa chichikondi chanu chosasinthika akhululukireni anthuwa ntchimo lawo monga mwakhala mukuwakhululukira kuchoka panthawa yomwe munachoka ku aiguputo mpaka tsopano, Yehova anawayankha kuti ndawakhululukira monga wapemphera” (18-20). “palibe ndimunthu modzi yemwe wa anthu amenewa amene adzawone dziko lomwe ndinalonjeza ndi lumbiro kwa makolo awo” (23). “Ine Yehova ndanena ndidzachitadi zimenezi kwa anthu onsewa omwe agwirizana kunditsutsa, adzathera m’chipuluru momwemuno adzafera mchipuluru momwemuno basi” (35).

Nkhani yomwe ikukambidwa apa ndiyakuti “Mose amapemphera mupemphero lake kuti Mulungu akhululukire ndikusaononga Israeli panthawi imene akazitape anabweletsa uthenga oyipa. ndipo mulungu anakhululukira Israeli Chifukwa cha Chifundo chake chachikulu kungakhale kuti anthuwa anali oyipa (anakhalabe oyipa kufikira kuti anthu onsewa adafa muchipululu). Tawonani (1) zikuoneka kuti Chikhululuko chomwe mulungu anaotsetsa apa ndi Chosapulumutsa (kungakakhale kuti mulungu anawapulumutsa kuchiweruzo chake pa Nthawi imeneyo, koma onse adathera muchipululu). (2) Mose mupemphero lake anapempha nati Mulungu ndi wa Chifundo ndi wokhululuka monga mwachikhalidwe chake kungakhale kwa anthu awa okanidwa.”

Munthu ofunsa wabweletsa nkhani yofunikira kwambiri. osati ku buku la Numeri lokha komanso kumagawo ena a M’buku lopatulika, apa zikuoneka ngati mulungu, akulonjeza Chipulumutso ndi kupeleka chiwopsezo cha Chilango cha Muyaya kwa anthu awa ,nkhaniyi silichoncho. Mulungu sangakhululukire anthu kenako mkuwapititsa ku Gehena. ngati mulungu anakhululukira anthu onse anachimwa ku kadeshi pamene Yoswa ndi kalebe anabweletsa uthenga komanso pakukana kulowa ku kenani anthu onsewa sakanafera muchipuluru. Tili pomwepo kumbali ina, kukanakhala kuti anakanthidwa ndi Chilango cha Mulungu ndiyekuti sanakhululukidwe. kukhulukidwa kwa Machimo ndikowoonadi. Ngati mulungu wakhululuka machimo a Munthu zikutanthawuza kuti Mulungu wamulungamitsa munthuyo kuti sakuyenera kulandira Chilango chake.

Munjira ina iliyonse tikuyenera kudziwa kuti Kulibe Chikhulukiro cha Mulungu Chomwe chimatchedwa kuti “Chikhululukiro cha Mulungu chosapulumutsa” kuti tiyankhule motelemu zikhoza kumveka motere kukhululuka kosakhululuka kapena kunena kuti chipulumutso Chimene sichimapulumutsa. Ngati ondiweluza milandu wakhululuka ndiyekuti ndine Mfulu kuzotsatira zonse za M’malamuro kuti sindikuyenera kulandira Chilango pa mulandu omwe ndinapalamura, sindingaweluzidwenso ndi mulandu omwe ndinapalamura. Ngati ndingakatsekeledwe kundende komanso kulangidwa chifukwa cha Mulandu wanga ndiye kuti sindinakhulurukidwe.

Kapena kuti kuchedwetsa kwachilango ndi mtundu Umodzi wakukhuluruka kuti ochimwayo apitilizebe kuchimwa kuti pa mthawi yake adzalangidwe (Aroma 2:5) ngati kuchedwetsa kwachilango ndi mtundu wakukhuluruka ndiye kuti mulungu anakhara zaka 6000 akukhulukira anthu machimo awo alindicholinga choti adzawawononge. Ngati oweluza mulandu akusintha masiku oti Mulandu uweluzidwe sizikutanthawuza kuti wakhululuka zolakwazo koma kuti wangochedwetsa masikuwo kuti M’malanduwo uweluzidwe.

Kunena kuti Mulungu ndiwachifundo “pa Umulungu wake” ndizowona koma mulungu salichoncho  kwa anthu omwe ndi okanidwa, omwe akupita kuchiwonongeko cha Muyaya. izi zikanakhala kuti ndizowona, Mulungu akanakhala kuti akuzikana yekha, akukana chikhalidwe chake chachiyero pa nthawi imene akuwalanga kwa Muyaya.

Izi sizikuyankha funso loti kodi Mulungu amapanga bwanji zinthu zake,kunena kuti Mpweya omwewo ukuyankhura zakukhululuka ndi Chiweluzo cha iwo omwe achimwa. Yankho ndilakunena kuti mulungu sakuyankhura kwa munthu modzi koma ku Mtundu wa anthu aku mpingo wachipangano chakale (Machitidwe 7:38). Mtundu umenewo mpingo wachipangano chakale, monga zili mu mpingo wachipangano chatsopano omwe muli gulu la anthu osiyanasiyana. Mumpingo muli anthu omwe machimo awo anakhululukidwa kwa muyaya ndiponso mu mpingo momwemo muli anthu omwe machimo awo sadzakhululukidwa kwa Muyaya pa chiweruzo cha Mulungu. Chifukwa chakunena kuti anthuwa ndi osakanikizana mulungu akuyankhula kwa onse, kulonjeza chikhululuko komanso Chilango Chamuyaya, ndipo mawuwa akukomera kwa iwo omwe ali osankhidwa ake a Mulungu ndi opulumutsidwa ndi Mwazi wa Yesu.

Chiphunzitso ichi chimapezeka mu Buku la Aroma 9:6-7:  “sikuti mawu amulungu analephera. pakuti si onse obadwa mwa Israeli amene ndi Israeli. Kapena kuti ana ake chifukwa anachokera mwa Abrahamu. koma zidzukulu zako zidzachokera mwa Isaki.” kuti tiwonetsetse Paulo akukakamira kuti mawu a Mulungu salephera, Zimene zikuonetsa kuti nkhaniyi palibe chomwe chikulephera mawu akukhululuka machimo ndi chiweluzo zonse zikuchitika pamodzi. pamene mulungu akuyankhu zachikhululukiro sakuyankhura kwa iwo omwe akungo kutchedwa kuti ndi a Mtundu wa Israel chabe koma mbewu yomwe inalonjezedwa yosakhidwa kuchokera mwa Abrahamu, ndipo iwowa siwongotchedwa chabe ana Abrahamu komanso ana amulungu okondedwa omwe machimo awo anakhulukidwa kudzera pa mtanda.

Nthawi zonse pa mpingo pamapezeka iwo amene amapembedza limodzi ndi anthu okhulupilira chowonadi, ndipo anthu amenewa kumakhara kovuta kuti asiyanitsidwe ndi iwo amene ali okhulupilira koma iwo amakhalara kuti Sali Thupi la Yesu khristu. “umene ndi thupi lake, chidzalo cha iye amene adzaza chilichonse mu njira iliyonse” (Aefeso 1:23). Iwo amene ali mwa iye amapeza mtendere ndi chikhulukiro, koma onse amene amabisara ndi kusakhulupilira samapeza mtendere ndi chikhululuko. “N’chiyani tsopano? chimene Aisraeli anachifuna ndi mtima wonse sachipeze koma osankhidwawo anachipeza. Enawo anawumitsidwa Mtima,monga kwalembedwa kuti Mulungu anawapatsa Mzimu wosatha kumvetsa zinthu,maso osatha kupenya;makutu osatha kumva mpaka lero lino” (Aroma 11:7-8)

Kodi zikutanthawuza kuti Uthenga wakhululukira machimo sumagwira ntchito kwa iwo omwe akutayika? sizikutanthawuza choncho. iwo amene akutayika akuyenera kumva mawu a uthenga wa chikhululukiro kuti adziweluze okha .Mulungu ali “pachikhalidwe chake” Mulungu ndiwa chifundo, kulalika za chifundo chake kwa aliyense zimapangitsa kuti onse omwe amamva ndikusakhulupilira chifundo chake kumawapangitsa kuti akhale ndi mlandu pa maso pake ndikutinso akhale oyenera pachiweluzo chake.

Kodi zikutanthawuza kuti uthenga wa Mulungu wa chiweluzo sumagwira ntchito kwa iwo omwe akhululukidwa machimo? ayi. uthenga wachiweruzo ukuyenera kupita kwa iwo omwe machimo awo akhululukidwa, osati kuti adzakhala pa chiweruzo chamulungu kwa Muyaya (Mayamiko apite kwa iye chifukwa cha Mphatso ya Mwana wake) koma chifukwa chakuti iwo anachimwa akuyenera kulapa ndikusiya machimo awo, monga kudzera mwachisomo chauzimu chosakanidwa.

Uthenga wa Mulungu wa chikhululukiro ndi wachiweruzo cha Machimo umapita kwa iwo onse omwe akumva mawu, ndipo ndi mawu amene amagwira ntchito kufewetsa, kulimbitsa ndikubweretsa chiweruzo chamulungu kwa omwe amatchedwa ana Isreali kapena akhristu ndiponso amabweretsa mtendere ndichikhululuko kwa iwo amene anasankhidwa molingana ndichisankho Chamuyaya kudzera ku mwazi wa khristu ndi ntchito ya Mzimu Oyera, Iwo ndi ana ake.

Show Buttons
Hide Buttons