Rev. Ron Hanko
Modzi mwa iwo amene amawerenga nkhanizi anatumiza pempho ili: “ndimafuna ndifunse ngati kungatheke kulemba nkhani yosiyanitsa ndi kufananitsa pa zinthu izi Kupanga ubwenzi ndi dziko lapansi Zimene zili udani ndi Mulungu, komanso Kupanga ubwenzi ndi anthu osakhulupilira ngati njira imodzi yakulalikira uthenga wabwino kwa anthu osakhulupilira (Life on Life and Word of Witness)”
Chinthu chimodzi chomwe chili chokhudza apa ndicho chikutchedwa kuti “Kupanga ubwenzi kuti mulalike uthenga wabwino” (friendship evangelism), koma choyambilira zokhudzana ndi utumiki otchedwa kuti Liwu la umboni wa Moyo (Life on Life and Word of Witness) utumiki wakale omwe ukutchedwa kuti Life on Life Ministries ndi utumiki omwe uli olumizikidwa ndi mpingo wina omwe umapezeka ku Mzinda wa Georgia ku United States. sindikudziwa kuti munthu amene anafunsa funso la lembedwalo kuti amathandawuza chiyani pamene anati Liwu la umboni wayo (Life on Life and Word of Witness), sindinapeza umboni wina uliwonse wa zomwe amakambazi ndikungoganiza kuti ndi Bungwe lina lomwe likufanana ndi otumiki otchedwa kuti Life on Life (Moyo pa Moyo).
Ma Bungwe onga awa a life on life ndi omwe akumaoneka ngati achikhristu masiku ano, Cholinga chawo chenicheni ndikulalika uthenga omwe okumakhudzana ndi kudzikhutitsa wenkha ndi Moyo oyang’ana za iwe Mwini, kudzimva kuti ndiwe ofunikira komanso wabwino ndikuyang’ana m’mene ungadzikhutitsire pa umunthu wako ndi kuzisangalatsa pa wekha. Palibe Chimene akumakamba chokhudzana ndi tchimo, Chisomo ndi chipulumutso chakudza kudzera muchikhulupiro chokha mwa Yesu Khristu. Utumiki wa Life on Life kudzera pa website yawo anayamikira Buku lomwe linalembedwa ndi Tsogoleli yemwe anayambitsa utimikiwu lomwe mutu wake umati: “kodi ndinu okhumudwitsidwa kuti Moyo wanu okusowekera kukhutitsidwa kwa Muyaya? (“Are you frustrated that your life lacks lasting satisfaction?”) Tilimu nthawi imene anthu akusakasaka thandauzo, Cholinga ndi kukhutitsidwa, ndipo akukhumudwitsidwa, ndikusweka mtima ndi kuthedwa Nzeru chifukwa cha uthenga wachinyengo omwe ukumapeleka malonjezo koma osakwanilitsa. kusowekera kwa kusankhutsidwa kunafikira zaka zonse zakale, Mitundu ya anthu komanso ndi Muzikhulupiliro. sikawiri kawiri kuyunkhulura ndi anthu omwe amanena kuti ndiwolimba Moyo wa uzimu koma samadziwa kuti angakhale bwanji Moyo ukhutitsidwa. Muyankho ‘lomwe anapereka’ Randy Pope akutiyitana kuti thitha kupeza cholinga chachikulu komanso kukhara Moyo wokhutitsidwa.” kungakhale kuti Yesu khristu akutchulidwa mu website yi, sindinapezeke uthenga Umodzi omwe ukukamba za uchimo ndi Chipulumutso. Life on Life ndi Utumiki chabe omwe ukukamba uthenga oti “anthu adzingomva bwino” umene suli uthenga wabwino konse wa Ambuye wathu Yesu khristu okhudzana ndi Manzunzo, imfa ndi kuwukitsidwanso kwa Yesu.
Bungweli ndizovuta kuti tidzilitchura kuti ndi lachi Khristu. ndi ongokhudzana ndi kudzikutitsa iwe Mwini ndi kudzikwanilitsa ndipo sayelekeza kungakhale kunamizira kulalikira uthenga wabwino wachisomo. Akhoza kutsutsidwa pa mfundo zambirimbiri: kusowekera kwawo posalingalira kuti Buku loyera limati chiyani zokhudzana ndi Utumiki ndi mayitanidwe a iwo omwe anayitanidwa kuti akalalikire za uthenga wabwino wa Yesu Khristu, Pamowonedwe awo ochepekera pa nkhani ya kukhara Moyo okhutitsidwa ndi chimwemwe cha pa iwe mwini, Kusamvetsetsa kwawo pa zofunikira zathu za Moyo wa uzimu komanso kukhazikika pa chiphunzitso chakuti anthu adzimva bwino, koma vuto lalikulu ndi “Ma Utumiki” awa ndiwakuti mwa Iwo mulibe uthenga wabwino wa Ambuye wathu Yesu nkhristu, amangochita Utumiki wapakamwa kwa Khristu yesu ndi ntchito zake za Chipulumutso.
Kutchulidwa kwa Bungwe monga la Life on Life Ministries wandipatsa mwayi oti ndilembe za Chinthu chinachake chomwe chakhala chikundivutitsa kwa mthawi yayitali, ndivutonso lomwe lakhalapo osati pa ma utumki “ongomvetsa bwino” komanso Matchalitchi kapena mipingo Ya Chi evangelical. ndikukamba nkhani yakunena kuti aliyense mu tchalintchi, M’khristu aliyense akuyenera kukhara ndi Utumiki wina wake kuti akathe kukhara Moyo okwanilitsidwa. Utumiki wa munthu okhoza kukhala china chilinchonse kuyambira kugawa timabuku, kugogodazitseko, kupita maiko ena kukalalikira, (ndipo nthawi zambiri kubwera mutakhumudwitsidwa, kufoowoketsedwa, kufunsa chikhulupiliro chako chomwe). Zotsatira zake zimakhara zakunena kuti Mautumiki amadzadza ndi Atumiki oyimba nyimbo, atumiki otumikira omwe Salipa Banja, Azitumiki awana, Atumiki Achinyamata, ….ndi ena ambiri. Ndiye Chimene chimachitika ndichakuti anthu amumpingo amaganiza kuti ngati salindi Utumiki winawake amaganiza kuti iwowa ndi otsalira amumpingowo.
Choyiwalika ndichakuti Chowoona chamu Baibulo ndi chakuti mpingo ulindi Utumiki Umodzi okha, kulalikira uthenga wabwino wa AmbuyeYesu Khristu, Paulo anati kwa iye mwini “ngakhale ndili wang’ono pakati pa anthu onse Amulungu, anandipatsa Chisomo chimenechi cholalika kwa anthu amitundu ina chuma chopanda malire cha khristu.” (Aefoso 3:8) kwa Timoteyo anati “lalikila Mawu khala okonzeka pa mthawi yake ,ngakhale pamene si pa nthawi yake. konza zolakwa zawo, dzudzula ndipo limbikitsa moleza mtima kwambiri ndi malangizo osamalitsa” (2 Timoteo 4:2).
Chinthu china choyiwalidwa ndichakuti pali lamuro la M’malemba kuti wonse omwe akukalarikira mawu akuyenera kutumizidwa monga Paulo adatumidwa, (Mac 13:1-3) “ndipo adzalalika bwanji ngati sanatumidwa? Monga kwalembedwa akongoladi mapazi a iwo amene amabweretsa Uthenga wabwino!” (Aroma 10:14-15). kutumidwa kumeneku kumachitika ndi Mulungu kudzera ku Mpingo, ndipo kumatsatana ndikusanjikiza manja kapena kudzodza komwe kumachitika ndi Mpingo.
Chinanso choyiwalika pakuonongeka kwa Mabanja, M’manyumba ndi tchalitchi ndizowona kuti Mulungu watiyitana kuti tikatumikire M’malo amene watipatsa, ngati Azibambo ndi Akazi, Makoro ndi ana amene tatanganidwa ndi ntchito zathu zatsikunditsiku, chinachilichonse tikuchitacho. Paulo amene amalimbananso ndi zithu zina zomwe tikuziwona pano, akuti “Abale, aliyense angokhala pamaso pa mulungu monga momwe analili pamene Mulungu anamuyitana” (1 Akolinto 7:24). ngati ndine okwatira komanso ndili ndi ana ,udindo wanga oyamba komanso wa ukulu ndi Mkazi wanga ndi Banja langa ndipo sindikuyenera kusiya udindo umenewu Chifukwa cha “Utumiki.”
Sichokhacho ndikuyenera kumvetsa kuti zili mumayitanidwe omwe mulungu anandipatsa, ine ndi Mboni yaikuru ya Yesu Khristu. Makamaka mudera limene tikukhara lomwe likumaona kuti Banja lilibe thandauzo lililonse. kumene Moyo wa M’banja ndichipsinjo, kumene chowonadi ndi luntha zikumatayika, kukhulupilika kwanga kumadera ngati amenewa ndi umboni wabwino kusiyana ndikugogoda pakhomo la munthu.
Ndikuyenera kuti ndimvetsetsenso kuti kusintha kwakaonedwe ka Mtchito kamati Mphunzitsa kuti, Ntchito yonse ya munthu okhulipilira, ntchito ya Mzimayi pakhomo, ntchito ya Bambo yothandizira Banja lake, ntchito yonse, kayandiyosafunikira kapena ndiyaying’ono bwanji ndiyodalitsika ndimulungu ndipo imagwilitsidwa pakuonetsa ulemelero wake wa Yesu khristu, pokulimbikitsa ndi chipulumutso cha ena, komanso kutipatsa mtendere wathu ndikutikhutitsa. zimayi sakuyenera kuganiza kuti kuchapa dzovara ndikutsuka Mbale ndi tchito yaing’ono kuti akuyenera kupeza Utumiki wina wake kuti akhale okhutitsidwa. koma akuyenera kudziwa kuti Yesu amayipanga kukhara ntchitoyo ya iye mwini, amaidalitsa ndikuigwilitsa ntchito koponso momwe tikuyembekezera. ndichifukwa chake mawu aku 1Akolinto 7:24 akuti “ndi Mulungu” ndipo ndichifukwa chani Paulo akutilimbikitsa, choncho, abale anga okondedwa imani njii. Musasunthike ndi chiliconse. Nthawi zonse mudzipereke kwathunthu ku ntchito zanu mwa Ambuye sizili zopanda phindu (15:58). ntchito ya Ambuye sikulalikira kokha ndi kuchitira umboni, komanso kutchetcha, kutora zinyalala, kukhoma misomali, Kupanga ntchito zowelengera ndalama, pamene zikuchitika chifukwa cha Yesu, ndi Pemphero ndi chikhulupiliro.
Sindinakhudzeko za kupanga ubwenzi ndiwanthu ngati njira yolalikira uthenga wabwino, ndikukhulupilira kuti anthu athu owerenga atipatsa mpata ndipo adikira zochuluka pa Phunzilori.