Menu Close

Mulungu Osasintha / The Unchangeable God

     

Rev. Angus Stewart

(1)

Kusintha ndi gawo la m’katikati Mwachilengedwe chathu ndi Dziko lakugwali, Kumakhara kusintha kwa Nyengo, Kwachuma komanso ndikusintha kwa zinthu zamakono. Zinthu zina zomwe zimasintha Mmayaiko makamaka zimakhara zokhumudwitsa ndi zowawa: Nkhondo, Matenda ndi Njara, Tingonena kuti pafupifupi nkhani zambiri zimakhara nkhani yazakusintha.

Tangoganizani zakusintha komwe kumachitika pa Moyo wanu. Munali kamwana kakang’ono musanabadwe M’mimba mwa Amayi anu, Patatha miyezi isanu ndi inayi munabadwa, munakura kuchoka ku Umwana kufika mutakulako pang’ono musanafike dzaka Makumi awiri kenakono Munakura nkukhara munthu wankuru. Kuukulamba wathu tsisi limayamba kuchepa kungakharenso kuthothoka kumene ndipo Mphamvu zathu zimatha.

Kumakhara kusintha pa Moyo wa Banja lathu, kuwasiya Makoro athu kupita kumaphuziro aku sukulu za Ukachenjede, Kapena kugwira ntchito yathu yoyamba. Moyo wa Munthu umakhudzana ndikukwatira, kukhara ndi Ana kenakono timawawona akuchoka pa Nyumba kupita ku Banja pakapita zaka zambiri timakhara ndi zidzukuru, timakumana ndi imfa, kungakhalenso kunkhara Mzimayi wa Masiye omwe mamunake anamwalira. Kumakharanso kusintha kwina monga, osapeza ntchito, Mavuto okhudzana ndi thanzi, kwa inu, okondewa anu kapena nonse kukhara odwara!

Timakumanaso ndi kusintha kwa kukuru, zobweza mbuyo ngakhalenso zopititsa Moyo chitsogoro, m’mene timvelera: Mkwiwo, kukhumudwa, kukhara osasangalara, kukhumudwitsidwa, Mthawi zina timakhara tokha Chete, Timalimbikitsidwa, kuthandizidwa kapena kukhara okondwera wina ndi mzake. kungakhalenso ubwezi wathu ndi Mulungu amene anatipulurumutsa pa mthawi ina timakhara naye chifupi nthawi zina timamutalikira.

Munthu yemwe analemba Masalimo 102 analemba zinthu zambiri zokhudzana ndi kusintha. Mawu otsogolera amati Pemphero la munthu wosautsidwa pamene walefuka, nakhuthulira pamaso pa Yehova kulira kwakeko. Adali kusekedwa ndi “Adani’’ (8) ake ndipo anali akukumana “ndimavuto” pakuti Masiku anga akupita ngati Utsi ,Mafupa anga akunyeka ngati Nkhuni zoyaka, Mtima wanga wakanthidwa ndipo ukufota ngati Udzu, ndipo ndimayiwara kudya chakudya changa,chifukwa chakubuwura kwanga kofuwula ndatsala chikopa ndi Mafupa okhawokha (3-5).

Dzanja la mphamvu la Mulungu linali pa iye. Anali m’chisoni ndi kulira chifukwa cha ichi “chifukwa chaukari wanu wa Ukulu mwandinyamura ndikunditayira kumbali” (10). Mumagawo osiyanasiyana Masalimo akuwonetsa kuti Mpingo Nthawi imeneyo unali kukumananso ndinyengo zovuta. Chitonthozo chonse chomwe anachiwona wolemba masalimoyu chinali chifukwa chakunena kuti chikhalidwe chamulungu ndi Chaphumphu: Mulungu ndi osasintha muchikhalidwe chake kapena kuti Ndiokhazikika. izi zikupelekanso Malangizo kwa Ife.

Apa kusasintha kwa Mulungu kukuonetsedwa mwa lunso kwambiri, osati mongotsutsana ndikusintha kosakhazizikika kwa olemba Masalimo ndi anthu amu Mpingo, komanso motsutsana ndi zinthu ziwiri zomwe zimaoneka ngati zokhazikika komanso zosasintha pa dziko la pansi, Kodi zinthuzi ndi Chani? Dziko lomwe liri pansi pathu ndi Dziko lakumwamba lomwe liri pa mwamba pathu. Pansi pathu dziko ndilolimba komanso losatekeseka. Zinthu za padziko zimasintha mitengo imataya Masamba, Nyama zimafa ,nyumba zimangidwa pa nthaka zatsopano, koma dziko palokha silimasintha. kumwamba ndichitsanzo cha zinthu zosasinthanso. zoonadi mitambo imasuntha Mlengalenga, pamene Dzuwa, Mwezi ndi Dziko zimazungulira kunja kwa danga, koma Miyamba payokhayokha kwakukuru simasintha.

Komabe, kungakhale kumwamba  ndi Dziko zimasintha ,makamaka pachiyambi padzikoli ndi kumathero ake, kumwamba ndi dziko zinalengedwa ndipo zinaonekera kuchokera kuzinthu zosaoneka “Pachiyambi inu munakhazikitsa Maziko adziko lapansi ndipo mayiko akumwamba ndi ntchito za manja anu” (25). kumwamba ndi dziko lapansi zizasandulika pakubweranso kwa Yesu khristu kachiwiri: “izi zidzatha koma inu mudzakhalapo zidzatha ngati chovala ndipo zidzatayidwa koma inu simusintha ndipo dzaka zanu sizizatha” (26). Dziko silidzaonongedwa koma kupangidwanso mwatsopano ngati kumwamba kwatsopano ndi dziko latsopano (Yesa 65:17; 66:22; 2 Peturo 3:13; Chivumbulutso 21:11).

Kumwamba ndi dziko lapansi zinalengedwa ndi Mulungu wamphamvu osagwilitsa ntchito kanthu kenakalikonse (Salmo 102:25), ndipo lidzapangidwanso mwatsopano ndi ulemelero kumapeto kwakutha kwa dzikori (26), “koma inu simusintha” (27) popeza kuti Yehova ndi Mulungu wosasintha! Mulungu wamkuluku “ali yemweyo” M’mene analili munthawi yamuyaya Mulungu olenga amene ali osalengedwa. Mwachoonadi chenicheni sanasinthepo ndipo sadzasintha kunthawizanthawi. iye ndiosansintha chilengedwe chisanakhalepo, munthawi ya amene analemba buku la Masalimo, munthawi yathu ino, nthawi imene adzasandulitse kumwamba ndi dziko lapansi tsiku lomaliza. zinthu zonsezi zidzasintha koma iye aliyemweyo (26-27).

Yakobo anati “Mphatso ina iliyonse yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate wa mwini kuwala amene sasintha ngati mthunzi oyendayenda” (1:17) akatswiri oyangana zamulengalenga amagwilitsa ntchito zinthu zosintha, kungankhale Nyenyezi zimasintha zimakula ndikuchepa, koma Mulungu aliyemweyo “samasintha” Mawu akuti kutembenuka kwa chinthunzithunzi anachokera ku dziko la anthu omwe amamapanga kawuniwuni wa zamulengalenga, zolengedwa za mwamba monga mwezi zimaonetsa chinthunzinthunzi, koma mulungu samasintha ndipo alibe chinthuzi chomwe chimatha kutembenuka. ndipo pazonse ndiye Tate wakuwara. iye ndiye mulungu amene ali wosatha konse wodara ,waphumphu modzi yekhayo “Mulungu ndiye kuwara mwaiye mulibe mdima” (1 Yohane 1:5) ndi Mulungu amene alikuwala ndi Tate wakuwala, Mwa iye mulibe kusintha kungakhale ndikupezeka ndi chithunzithunzi chomwe chimatembenuka, popeza kuti iye ndi owona ndi osansintha.

Malaki 3:5 imakamba za M’chitidwe woyipa wa Israeli, wamatsenga,chigoloro, kulumbira za bodza, Mkhanza, ndikusamuopa Mulungu, tikhonza kuphatikizanso machimo onse omwe mpingo wakhala ukuchita mudzaka nzonse, kuphatikizaponse ndizolakwa zathu, pakanakhala kuti panali chifukwa chomwe mulungu chikanamupaningitsa kusintha pakusiya kukonda thupi lake omwe uli mpingo ndikuyamba kuwuda, ndizimenezi. Koma timawerenga kuti chani? “pakuti ine ndi Mulungu sindimasintha, kotero kuti inu ana a Yakobo simunawonongeke” (6). Uwu ndi umboni weni weni wakuti Mulungu moyo ndi choonadi ndi Mulungu osasintha! Chipulumutso chathu mwa Yesu khiristu ndichotsimikizika, mwa Mulungu wa osankha mwa muyaya, Chiwombolo Cha chikondi ndi kubadwanso mwatsopano kosakanidwa sizidzasintha.


(2)

Kupatura Ma verse ena apaderadera ku Masalimo 102:27, James 1:17 and Malachi 3:16 anagwilitsidwa ntchito ku nkhani zapita (Mulungu osasinthika gawo 1) Pali dzina limodzi la Mulungu lime limaphunzitsa za kusasintha kwa Mulungu, Mukulidziwa dzina limeneli? Yehova!

Dzina la Yehova likuchokera ku M’neni wa Chihebeli “Kukhala” ndi dzina la Umulungu lomwe Ngelo wa Ambuye anamufotokozera Mose pa nthawi imene chitsamba Chinkayaka Moto Pa Phiri la Sinai: “Ndine amene Ndili” (Ex. 3:14) inu ndi ine sitingathe kudzitchura tokha opanda fano loyipa. Ngelo Gabrieli sangathe kunena ichi, Palibe cholengedwa chili chonse chomwe chingathe kudzitchula dzinali. Koma Mulungu Yekha wamphamvu akhoza! iye ndi wamuyaya ndipo aliyekha mwini, ali Chimene anali, ali ndipo adzakhara: Kulibe anamulenga, wachowonadi, osasintha “Ndine amene Ndili.”

Tayiyeni tilumikizitse dzina limeneli ndi Malemba omwe tinatchula kumayambiliro. “Pakuti ndine Ambuye (Yehova, wosasintha, Ndine amene Ndili, kotero kuti” sindimasintha (Malaki 3:6) zokhudzana ndi iye mwini ngati Yehova akuti “Ine ndine amene ndili” ndipo mpingo umavomera ndikupembedza “inu muli Yemweyo (Salmo 102:27) ngati Yehova amene muli mthawi zonse mpaka kale ndipo simusintha Chimene muli, Yakobo 1:17 Mosabisa akumutcha kuti “Tate wakuwara, mwa iye mulibe kusintha kungakhale kutembenuka kwa chinthunzithunzi.”

Kupatura ma verse apadelera a M’malemba (makamaka atatu omwe atchulidwa kawiri Mwambamu) ndi dzina la Mulungu la Yehova, pali chinthunzithunzi chomwe chimagwilitsidwa ntchito pomufotokoza mulungu Kuti samasintha “Iye ndi Thanthwe.” Monga David anati “Yehova ndi Thanthwe langa, Chitetezo changa, ndi Mpulumutsi wanga, Mulungu wanga ndi Nthanthwe langa m’mene ndimathawiramo chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa ndi linga langa” (Salmo 18:2)— kungogwitsi chitsanzo chimodzidzi kuchokera M’malemba. Ambuye wachipangano chathu ndiwokhazikika, Sasiyiza, wamphamvu, odalirika, okhulupilika, ndi osasintha ngati Thanthwe!

Mulungu wathu sinanzikambe amene amasintha ndi zomwe zamuzungulira, iye chinthawi chomwe chimazungulira ndi Mphepo. “iye ndi Thanthwe losasintha.” ndipo ntchito zake zonse ndi ndi njira zake zonse ndizaphumphu zachilungamo ndi zowongoka (Det. 32:4) ndimafuna ndingokupatsani chitsanzo chimodzi Chimene chikuwonetsera chifukwa chimene Mulungu akuyenera kukhara osasintha, ngati Chinthu chimayenera kukhala chosintha ndiye kuti chikuyera kusintha kuti chikhale chabwino kapena choyipa. koma mulungu sangasinthe kuti akhale wabwino iye ndiwangwiro kale mowonadi. ndipo iye sangasinthe kuti akhale oyipa ndiye kuti akhoza kukhala opanda ungwiro wa choonadi.

Mwachidule tingonena kuti Choonadi chakusasinthika kwa Mulungu ndi choonadi chenicheni chomwe chili chofunikira, ndimophatikizanso ndi MMaganizo awa Yehova ndiye wa ulemero osatha.

Potero kuti pamene mulungu anadziwonetsera Yekha kwa Mose, anati, Dzina langa ndine Yehova pakuti “Ndine amene ndili” (Exod 6:3; 3:14)!

Mulungu ndi wosasintha Muchani? ndiwosatha mwa iye mwini. zimenezi zikuphatikiza, choyamba ndiwosasintha pa Umunthu wake. Yehova ali mwa Atatu, ali Mulungu modzi mwa Atatu, Mulungu Tate, Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu, ndipo ali ofanana mu Mphamvu ndi mu ulemelero, okhara malo apangano la M’dalitso mpaka Muyaya.

Mulungu sanakhala mu Utatu pakulenga, kapena kudzera mukubadwa kwa Mwana ku thupi, kapena tsiku la pentekositi, Pamene Mzimu Oyera anapelekedwa ku Mpingo wa khristu wachipangano chatsopano. Mulungu ali atatu—Tate, Mwana ndi Mzimu oyera—wamuyaya ndi osasintha, Monga akunena kuti “pakuti ndine Ambuye sindimasintha” (Mal 3:6).

Chinthu chachiwiri mulungu samasintha muchikhalidwe chake. Mulungu samasintha molinga ndi mthawi kapena Malo, Pakuti iye ndi wa Muyaya, pakuti iye ndi opezekaponseponse. ndipo iye samachepa kapena kukura mu Mzeru pakuti iye ndiodziwa zonse. ndipo iye samaonjezera mphamvu kapena kufooka pakuti ndi wamphamvu zonse. ndipo iye sakula kapena kuchepa muchina chili chonse ndiwopanda malire. katekisima wa Westminster wa chidure anamaliza motere, “Mulungu ndi Mzimu, opanda Malire, wamuyaya, ndi osasintha, mwayi muli, Nzeru, chiyero, Chilungamo, ubwino, ndi choodadi” (A. 4). Timabweleza mwa ulemu mawu owuzilidwa ndi mphweya “inu muli yemweyo” (Salmo 102:27)!

Munthawi zonse pamene tikulimamba ndi chimphunzitso cha Aminianiasm, Tiyenera kulimbikira pakumphunzitsa kuti Mulungu samasintha muchikondi ndi chifundo chake, sizioona kunena kuti pa nthawi ina yake Mulungu amakonda ena ake pakamthawi kenakake, ndiye pamene munthuyo wafa, mulungu amamupanga kukhara M’dani wake, kenakono amamuponyera kugahena kwamuyaya.

Iwo amene Mulugu awakonda, amawakonda kwa Muyaya ndipo samasintha. Monga masalimo 136 imati motsindika kokwanira ka 26 “Chikondi chake ndi chosatha.” Mobwelizabweleza tikuyitanidwa kuti timuthokonze Yehova, Pakuti iye “anagonjetse Aiguputo mumwana wawo oyamba … ndipo adamiza pharaoh ndi ankhondo ake Munyanja yofiira … anapha Mafumu otchuka … Sihon Mfumu ya Amori ndi Og Mfumu ya Abashani,” (10, 15, 19, 20). Chifukwa chani? Chifukwa chakuti Chifundo chake ndichosatha! Palidalibe chifundo kwa Farao, Sihon, Og ndi anthu awo opemphedza Mafano, omwe adawagononga. Yehova ali ndichifundo kwa iwo anasankhidwa kudzera mwayesu ndipo amaonetsera chifundo ichi pakugonjetsa adani awo.

Aroma 8:38-39 imaphunzitsa mopitilira muyeso kunena kuti “palibe Chidzatilekanitsa ndi chikondi Cha Mulungu, Chimene chili mwa Ambuye wathu yesu Khristu”. Titatha kutchula zinthu zonse Zimene zikhoza kutilekanitsa ngakhale “imfa” zimenezi zikufikira dziko lonse kuti palibe “cholengedwa chili chilichonse chingatilekanitse.” Chikondi cha Mulungu ndi cha Muyaya komanso ndi chokakamira ndi chosagonjetseka. ndipo ndife awumodzi ndiye Mpaka Muyaya! ndiponso tikuwona kuti chitonthozo chathu chili mwa Tate wapangano lanthu lachoonadi mwa Iye “Tate wakuwara, mwayiye mulibe kusintha, ngakhale mthunzi woyendayenda” (Yakobo 1:17).

Kodi mulungu wamkulukulu Amakonda ndani? Amadzikonda iye mwini mosasintha (Mwapamwamba kwambiri), Mwana wake obadwa yekha ku thupi ndi onse osankhidwa mwa Yesu khristu. amatikonda mosasintha ndi amatikonda mpaka kumapeto (John 13:1)!

Monga Yehova ali osasintha umunthu wake ndi chikhalidwe chake ,kuphatikiza muchikondi chake ndi Chifundo chake, iyenso ndi osasintha kumadalitso ake. Mulungu sadzasinthako muchikondwelero chake kapena muchimwemwe chake, pakuti iye ndiwopanda Malire ndi osasintha ku M’dalitso wa iye mwini. ndipo mulungu salemera kapena kukhara ndi Moyo ochuluka pakuti mwa Iye ndiwokwanira ndiponso ndi waphumphu Mpaka kale.


(3)

Mulungu wosasintha mwa Iye yekha (Sal. 102:27; Mal. 3:6; Yak. 1:17) alinso wosasinthika mu lamulo lake lamuyaya, Lamulo la Mulungu ndi dongosolo lake lamuyaya kapena cholinga chake chokhudza kumwamba ndi dziko lapansi, angelo ndi anthu, ndi zolengedwa zonse. Limaphatikizapo tinthu tating‟onoting‟ono tating‟ono tomwe timakhala pa dziko lapansili, pansi pa dziko lapansili komanso pamwamba pa dziko lapansili, chifukwa Yehova “akuchita zonse monga mwa uphungu wa chifuniro chake” (Aef. 1:11). Mawuwa akusonyeza kuti Yehova “akuchita zonse monga mwa uphungu wa chifuniro chake.” Monga momwe Westminster Confession imanenera, “Mulungu kuyambira kalekale anachita, mwa uphungu wanzeru ndi woyera koposa wa chifuniro chake, mwaufulu ndi mosasintha, anaika zonse zimene zidzachitika” (3:1).

Ponena za lamulo lamuyaya la Mulungu, dongosolo Lake lophatikiza zonse ndi cholinga chake, Malemba Opatulika amalengeza kuti, mofanana ndi Amene anaupanga kosatha, sichisintha. Yehova ananena kuti: “Uphungu wanga udzakhalapo, ndipo ndidzachita chifuniro changa chonse” (Yes. 46:10). Choncho, Yehova amatiuza kuti: N‟chifukwa chake lemba la Ahebri 6:17 limanena za “kusasintha kwa uphungu wake.” Kugwiritsa ntchito chinenero cha Yakobo 1:17, monga Mulungu Mwiniwake, palibe “kusinthika” kapena “mthunzi wotembenuka” mu uphungu Wake wamuyaya.

Lamulo losasinthika la Mulungu limaphatikizapo kusankha kwake kopanda malire kwa ena kuti apulumuke mwa Yesu Khristu ndi kutsutsidwa kwa ena ku chiwonongeko m’njira ya machimo awo. Ponena za kusankhidwa kwathu, lemba la Aefeso 1:4 limati Mulungu “anatisankha ife mwa iye [kutanthauza, Kristu] asanaikidwe maziko a dziko lapansi. Monga umboni wa kutsutsidwa, timatchula za “anthu osapembedza” aku Yuda 4 “omwe anaikidwiratu kutsutsika kumeneku kuyambira kale.” Chitsanzo chodziwika bwino cha m‟Baibulo cha kusankhidwa ndi kutsutsidwa ndi cha mapasa a Isake ndi Rebeka, Yakobo ndi Esau. Anyamata aŵiriwo „asanabadwe‟ ndipo „asanachite chabwino kapena choipa,‟ kuti akwaniritse “chifuno cha Mulungu,” ichi chinali chifuniro Chake chamuyaya: “Ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau” (Aroma 9:11, 13).

Chifukwa cha lamulo laufumu wa Mulungu, chiwerengero cha osankhidwa ndi otayika sichingasinthe. Pali chiŵerengero cha “zotengera za mkwiyo zoyenera chiwonongeko” ndi chiwerengero china cha “zotengera zachifundo, zimene anazikonzeratu ku ulemerero” (22-23). Westminster Confession 3:4 njolondola: “Angelo ndi anthu ameneŵa, okonzedweratu ndi kukonzedweratu, analinganizidwa mwapadera ndi mosasintha; ndipo chiŵerengero chawo
n‟chotsimikizika ndi chotsimikizirika, kotero kuti sichingachuluke kapena kuchepetsedwa.”

Mayina a osankhidwa ndi oletsedwa nawonso sasintha. Mayina a okonzedweratu ku chipulumutso analembedwa m‟buku la moyo la Mwanawankhosa “chikhazikitso cha dziko lapansi” (Chiv. 13:8; 17:8). Kumbali ina, Yudasi, mwachitsanzo, nthawi zonse, pamaso pa Mulungu, “mwana wa chitayiko,” ndiko kuti, mwana wa gehena (Yohane 17:12).

Kusasinthika kwa Mulungu sikumangofuna kusasinthika kwa uphungu Wake wamuyaya, kuphatikizapo kusankhidwa ndi kutsutsidwa, komanso kumatipatsa umboni wotsimikizirika wa Umulungu wa Khristu. Salmo (102:25-27) likuchokera ku mawu pa (Ahebri 1:10-12) ponena za Ambuye wathu Yesu kuti: “Inu, Ambuye, pa chiyambi munakhazika maziko a dziko lapansi; ndipo kumwamba ndizo ntchito za manja anu: zidzatayika; koma inu mukhala; ndipo iwo onse
adzakalamba monga malaya; ndipo monga chovala mudzazipinda, ndipo zidzasinthidwa: koma Inu ndinu yemweyo, ndipo zaka zanu sizidzatha.”

Mwana wamuyaya sanasinthidwe ndi kubadwa Kwake, pamene anadzitengera kwa Iye umunthu weniweni ndi wamphumphu. Komanso Mulungu Mwana sanasinthidwe ndi mtanda wake, pamene Iye anasenza chilango choopsa chifukwa cha osankhidwa ake chifukwa cha tchimo lawo. M’chenicheni, mtanda ndiwo chisonyezero chaulemerero koposa cha kusasinthika kwa Mulungu. Chilungamo chosatha cha Yehova chimafuna chikhutiro, ngakhale chitakhala Im‟malo otetezera imfa ya Mwana Wake wobadwa ku thupi. Chifundo chosatha cha Mulungu sichisintha, kuphatikizapo chifundo chake kwa anthu ake okondedwa mwa Yesu Khristu, osasinthika kotero kuti Yehova sanalekerere Mwana wake wobadwa yekha (Aroma 8:32).

Chiphunzitso chokongola cha m‟Baibulo chimenechi cha kusasinthika kwa Mulungu ndicho chitonthozo chathu. Choyamba, pangano la Yehova silisintha: “Ndidzakhala Mulungu wanu kosasintha, ndipo inu mudzakhala anthu anga osasintha.” “Pakuti mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzagwedezeka; koma kukoma mtima kwanga sikudzachoka kwa iwe, ngakhale pangano la mtendere langa silidzagwedezeka, ati Yehova wakuchitira iwe chifundo” (Yes. 54:10).

Chachiŵiri, (Salmo 102:27-28) limaphunzitsa kusasintha kwa Yehova (“Koma Inu ndinu yemweyo, ndi zaka zanu sizidzatha”) zimatsimikizira kupitiriza kwa mpingo (“Ana a akapolo anu adzakhalabe, ndi mbewu zawo zidzakhazikika pamaso panu inu”).

Chachitatu, mu pangano lake losasinthika, Mulungu wosasinthika amasunga osati mpingo wake wokha komanso wokhulupirira aliyense payekha. 2 Timoteo 2:19 amatitsimikizira kuti Yehova mwachisomo adzasunga aliyense wa Iye yekha (“maziko a Mulungu ali okhazikika, okhala ndi chisindikizo ichi, Ambuye azindikira iwo amene ali ake”) ndipo, chotero, tiyenera kukhala ndi moyo wachiyero kuchokera m‟chisindikizo ichi. chiyamiko (“Aliyense wakutchula dzina la
Khristu achoke ku chosalungama”).

Poganizira kusasinthika kwa Mulungu wathu, maitanidwe athu ndi chiyani? Choyamba, musadalire chilichonse m’dziko lino, kuphatikizapo “chuma chosadalirika” (1 Tim. 6: 17) kapena munthu wosakhazikika. Musadalire akalonga (Sal. 146:3) pakuti atsamira “bango lophwanyika” (Yes. 36:6). “Musakonde dziko lapansi, kapena zinthu za m‟dziko.” Chifukwa chiyani? Pakuti “dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; M‟malo mwake, chachiŵiri, dalirani mwa Mulungu (1 Yohane 2:15, 17).

Wautatu wovumbulidwa mwa Yesu Kristu, amene anatiwombola ndi mwazi wa pangano losatha. Dalirani pa Iye pa zinthu zonse zakuthupi ndi zauzimu. Pajatu iye ndi Yehova, “Ine ndine amene ndili” wamkulu, wosasinthika, wokhulupilika ku Mau ake ndi malonjezo l (Yes. 26:4; Ahebri 6:11-20).

Chachitatu, pamene tikusinkhasinkha ndi kukonda Mulungu wosasinthika, tiyeni tiyesetse mwa chisomo chake kukhala okhazikika ndi okhulupirika tokha: osati mphindi imodzi ndi kutsika m’tsogolo, osati wachisomo lero ndi mwano mawa, osati okoma mtima m’mawa koma osakwiya madzulo. M‟malo mwake, tiyeni tikhale ofanana: kukonda Yehova Mulungu wathu ndi mtima wathu wonse, ndi mnzathu mmene timadzikondera ife eni mosalekeza. “kotero, abale anga
okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye nthawi zonse” (1 Akor. 15:58) Mulungu wosasinthika akulonjeza kuti, “Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo” (Chiv. 2:10).

Show Buttons
Hide Buttons